Home » Entertainment » Blantyre Press Club Igwirana Manja Ndi “Ma Blacks” Pothandiza Vuto La Kusefukira Kwa Madzi
Blantyre Press Club Igwirana Manja Ndi "Ma Blacks" Pothandiza Vuto La Kusefukira Kwa Madzi

Blantyre Press Club Igwirana Manja Ndi “Ma Blacks” Pothandiza Vuto La Kusefukira Kwa Madzi

Wolemba: Leo Mkhuwala

Blantyre Press Club Igwirana Manja Ndi “Ma Blacks” Pothandiza Vuto La Kusefukira Kwa Madzi

Pofuna kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi, bungwe la atolankhani la Blantyre Press Club (BPC) pamodzi ndi gulu loimba nyimbo za Reggie lomwenso ndi lotchuka la Black Missionaries, akonza dansi yomwe cholinga chake nkupeza ndalama zoti zithandize anthu omwe akhudzidwa ndi vuto la kusefukira kwa madzi.

Mbali zonse ziwiri zatsimikidza kuti dansiyi iripo Lachisanu lino, pa 22 Malichi ndipo ichitikira ku Mibawa Multi-Purpose Hall ku Limbe kuyambira nthawi ya 8 koloko usiku.

Poyankhulapo pa za chikonzerochi, Pulezidenti wa bungwe la BPC, Blessings Kanache wati, ndi cholinga cha bungweli kuti mamembala ake omwe ndi atolankhani atengepo gawo mwamsanga pochepetsa mavuto omwe anthu okhudzidwa akomana nawo.

“Omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi ndi Amalawi choncho ifenso atolankhani ndi Amalawi komanso iwowa ndi abale ndi alongo athu, choncho tikuyenera kukangalika ndi kuwathandiza,” anayankhula motero Kanache.

Poyankhulapo ku mbali yake, Ras Harawa yemwe ndi mkulu woyang’anira gulu la Black Missionaries wati, zonse zokonzekera dansiyi ziri n’chimake.

Iye wati bandiyi yakonzeka kwambiri kutsangalatsa anthu kudzera m’maimbidwe ochititsa kaso.

Harawa anapitilira ndikuti, bandi yake yomwe imatchuka kwambiri mwachidule kuti “ma Blacks” ndi yokondwa kugwirana manja ndi bungwe la BPC pa ntchito yothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi.

Malinga ndi akuluakulu a BPC, pali chiyembekezo choti dansiyi ipeze ndalama zotsachepera K3 Million.

Aliyense wolowa mu dansiyi adzalipira ndalama yokwana K2,500.

Ndalamazi ati agulire zakudya komanso katundu wina wosiyanasiyana yemwe bungwe la atolankhanili likapereke kwa anthu omwe akusowa thandizo la msanga m’maboma a Chikwawa, Nsanje komanso Blantyre.

Bungwe la BPC likuyendetsa ntchitoyi mogwirana manja ndi mabungwe ena monga bungwe la Red Cross.

Mwa ichi, pali chitsimikidzo choti ndalama zonse zomwe zipezeke zikafikiradi abale ndi alongo omwe avutika ndi vutoli.

Pakadali pano mabungwe osiyanasiyana komanso zipani za ndale ziri pa kalikiliki kupeza thandizo lokapereka kwa anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi m’maboma osiyanasiyana a m’dziko muno.

Maboma omwe akhudzidwa kwambiri ndi vutoli ndi a Chikwawa, Nsanje, Mulanje ndi Phalombe.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

MAAS organises art concert

MAAS organises art concert

Kwacha Studios Changed To Television Centre

Kwacha Studios Changed To Television Centre

WRASM advocating for wash services in Hospitals

WRASM advocating for wash services in Hospitals

error

Share Breaking News