Home » News » Papa Francisco Adzudzula Atsogoleri Andale Ouma Mtima Mu Uthenga Wake Wa Pasaka

Papa Francisco Adzudzula Atsogoleri Andale Ouma Mtima Mu Uthenga Wake Wa Pasaka


Wotanthauzira: Leo Mkhuwala

Papa Francisco Adzudzula Atsogoleri Andale Ouma Mtima Mu Uthenga Wake Wa Pasaka

Mu uthenga wake pa mwambo wa mapemphero a Lachisanu Loyera, mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse, Papa Francisco wadzudzula kolimba atsogoleri a ndale a mtima wa mwala omwe salabadira zipsinjo zomwe anthu omwe amachoka m’maiko mwawo pa zifukwa zosiyanasiyana akukomana nazo.

Chidzudzulo cha Papa Francisco chinaturuka pambuyo powerenga pemphero lomwe linakamba za anthu osauka, anjala, achikulire, ana omwe akuchitiridwa nkhanza komanso za chilengedwe.

Iye anadzudzulanso mchitidwe wodzembetsa anthu womwe ukuchitika m’maiko osiyanasiyana.

M’mapempherowo, Papa Francisco anatchula za mtanda womwe anthu omwe amachoka m’maiko mwawo pa zifukwa zosiyanasiyana asenza ponena kuti anthuwa amapeza zitseko zotseka chifukwa cha mantha ndi alendo komanso kweni kweni chifukwa cha mitima youma ya atsogoleri andale omwe kachitidwe kawo ka zinthu kamanga nthenje pa ndale.

Mwambowu womwenso umakwaniritsa zaka zisanu ndi ziwiri (7) akuchita nawo mwambo wa Pasaka chitengereni udindo wa Papa unayamba ndi mapemphero a “Njira ya mtanda” omwenso amadziwika kuti “Via Crucis” m’chiyankhulo cha Chilatini.

Pamwambowu, anthu zikwizikwi omwe ambiri ngochokera m’maiko osiyana siyana a padziko lapansi ananyamula makandulo oyaka.

M’mapemphero osinkhasinkha omwe anawerengedwa ndi anthu osiyanasiyankha m’magawo khumi ndi anayi (14) a njira yamtanda, omwenso amakumbukira maola omaliza a moyo wa Ambuye Yesu analembedwa ndi Sisiteri Euginia Bonetti wa zaka makumi asanu ndi atatu (80), wa m’dziko la Italy yemwe wakhala akupeza mphoto zosiyanasiyana kamba ka ntchito yake yothandidza anthu komanso ana omwe amachitiridwa nkhanza powadzembetsa.

M’mapempherowo, Sisitere Bonetti adalemba kuti:-

“Tiyeni tiganizire ana m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi omwe alibe mwayi wopita ku sukulu ndipo m’malo mwake, akugwiritsidwa ntchito ku migodi, m’ma esiteti ndi m’zintchito za usodzi pamene ena akugulidwa ndi anthu omwe amachita m’chitidwe wodzembetsa anthu ndi cholinga chofuna kuwachotsa ziwalo komanso kuwachitira nkhanza m’mizinda yosiyanasiyana ndipo ena mwa anthu akuchita izi ndi akhristu.”

Papa Francisco wakhala akuteteza anthu omwe amachoka m’maiko mwawo pa zifukwa zosiyanasiyana ngati phata la udindo wake ngati Papa.

Iye wakhala akudzudzula kolimba atsogoleri a ndale omwe salabadira anthu otere monga Pulezidenti wa dziko la America, a Donald Trump komanso nduna yoona za m’dziko ku Italy, a Matteo Salvini omwe amatsogolera chipani chomwe sichilola alendo kulowa m’dzikolo.

Mwa zina, a Matteo adatseka magombe omwe pamachokera komanso kufikira sitima ndi mabwato omwe amawagwiritsa ntchito yopulumutsa anthu ochokera m’maiko osiyanasiyana omwe amakhala pa chiopsezo chofera pa nyanja pa ulendo wawo wofuna kudzalowa m’dziko la Italy.

Papa Franscisco akuyembekezereka kutsogolera mwambo wa mapemphero ochezera a pasaka usiku wa Loweruka pa April 20, 2019.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

DPP Supporters In Mulanje Injured In Road Accident

DPP Supporters In Mulanje Injured In Road Accident

Sudan Protesters ✊Mourn Comrades Killed in June Raid

Sudan Protesters ✊Mourn Comrades Killed in June Raid

Wedding Bells For Journalists, Wesysylas Chirwa, Nancy Chumachawo

Wedding Bells For Journalists, Wesysylas Chirwa, Nancy Chumachawo

error

Share Breaking News