Home » News » Anthu Omwe Adavota Ku Limbuli Akuti Daudi Chida Ndi Mwana Wa M’mudzi

Anthu Omwe Adavota Ku Limbuli Akuti Daudi Chida Ndi Mwana Wa M’mudzi

Mtolankhani Wathu

Anthu a m’dera Mulanje Limbuli adzudzula m’chitidwe womwe gulu la anthu ena likuchita pomanena phungu wawo Daudi Abiyani Chida kuti sakuyenera kukhala phungu wa deralo kamba koti sadabadwire m’deralo.

Anthuwa, omwe ambiri mwa iwo ndi omwe atsimikiza kuti adavotera phunguyu pa chisankho chomwe chidalipo pa 21 Meyi, awuza mtolankhani wathu kuti: “Ndi nzopanda ntchito kumanena kuti ku Limbuli sikwawo kwa Daudi Chida pamene umboni wokwanira ulipo kuti kwa zaka zochuruka, phunguyu wakhala ali nzika wa deralo.

Motsogozedwa ndi mafumu, anthuwa ati makono, kumunena munthu kuti ndi “wobwera” ndi khalidwe la chikale lomwe likungowonetsa kusadzindikira kamba koti chomwe anthu amafuna pa munthu ndi chitukuko chomwe munthuyo amachita kudzera mu mphatso ya utsogoleri.

Masiku apitawa, potsatira kupambana kwa Chida ngati phungu wa dera la Limbuli, anthu ochokera ku mbali ya Graciano M’bawa yemwe amaima payekha pa mpikisano wa phungu wa deralo, adakhamukira ku ma ofesi a bwanankubwa wa m’bomalo ati kukapereka dandaulo loti sakumufuna Chida kamba koti sadabadwire m’deralo.

Kafukufuku wa Malawi Freedom Network pa nkhaniyi wapeza kuti, gulu la anthu, omwe akuti sakumufuna Chida pa mpando wa phungu, lidachita kutumidwa ndi M’bawa mothandizidwa ndi ena mwa anthu ochita za malonda omwe akhala akulimbana ndi Chida pa ndale monga a Chisomo Misoya, a M’meta komanso Gavanala wa DPP a Muonekeni.

Anthuwa akuchita izi posafuna kuvomereza kugonja pa chisankho chomwe anthu ochuruka adaonetsa chikhulupiliro chawo mwa Daudi Chida kuti akawaimilire kunyumba ya malamulo m’zaka zina zisanu.

Pa chisankho changothachi, Daudi Chida yemwe adaimila chipani cha DPP adapeza mavoti 17,548 pamene Graciano M’bawa adagonja atapeza mavoti 12, 093.

Pa chisankho cha mu 2014, Chida yemwe adaima payekha pa mpikisano wa phungu, adapambana ndi kugonjetsa phungu wa DPP yemwe adalipo pa nthawiyo, malemu Frazer Nihorya yemwenso adali wachiwiri kwa nduna ya zachuma mu ulamuliro wa Pulezidenti wakale, malemu Bingu wa Mutharika.

Potsatila kupambana kwake, Chida adalowa chipani cha DPP koma anthu a mbali ya phungu wakale, malemu Nihorya omwe ena mwa iwo ndi a M’meta, Misoya, Muonekeni ndi M’bawa akhala akulimbana naye phunguyu mu njira zosiyanasiyana, koma iye sanabwelere m’mbuyo maka pa ntchito yomwaza zitukuko zomwe mu kanthawi kochepa zasintha nkhope ya Limbuli.

Asanakhale phungu, Chida yemwenso ndi katswiri pa ntchito za malonda, wakhala akuchita malonda osiyanasiyana m’dera la Limbuli kwa zaka zochuruka.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

BOLA-CEFO Condemns Msundwe Protestors For Killing Police Officer

BOLA- CEFO CONDEMNS MSUNDWE PROTESTERS FOR KILLING POLICE OFFICER

Dowa To Fly MACOHA National Flag Week

DOWA TO FLY MACOHA NATIONAL FLAG WEEK

Strides Towards Peace, Reconciliation, Earns Ethiopian Prime Minister Nobel Prize

Strides Towards Peace, Reconciliation, Earns Ethiopian Prime Minister Nobel Prize

error

Share Breaking News