Home » Entertainment » FCB U20 iyamba ku Mzuzu • Oyendetsa akuti akuyembekezera mpikisano wamkulu kuchokera ku matimu

FCB U20 iyamba ku Mzuzu • Oyendetsa akuti akuyembekezera mpikisano wamkulu kuchokera ku matimu

Wolemba Aubrey Thom Vakhani

Matimu a Sanwecka ndi Mbahewe kuthambitsana muligi ya FCB U20
Kumwenda, Matimu a Sanwecka ndi Mbahewe kuthambitsana muligi ya FCB U20

Pamene ligi ya mpira wamiyendo ya anyamata achisodzera osapyola zaka makumi awiri (FCB U20) yayamba mumzinda wa Mzuzu Lamulungu lapitali pa 2 June, 2019, mlembi wamkulu wa Mzuzu Youth Football  Committee, Mwayi Mavado Kumwenda wati ali ndi chikhulupiliro kuti ligiyi ikhala yapamwamba kwambiri chakachino.

Kumwenda wati ngati komiti akuyembekezera mpikisano waukulu kuchokera ku matimu omwe akutenga nawo gawo muligiyi yomwe ikulandira thandizo la ndalama kuchokera ku First Capital Bank.

“Ligi yathu yayamba bwino kwambiri. Lero (Lamulungu lapitali) pokhala tsiku loyamba Taonga matimu akuonetsa mpira wabwino kwambiri zomwe zatipatsa chithunzithunzi ife oyendetsa ligiti kuti tikhala mpikisano waukulu pakati pamatimu,” anatero Kumwenda.

Iye anatinso mavuto okhudza oyimbira anawunikira ndipo sipakhala matimu kudandaula kwina kulikonse kuchokera kwa oyimbira.

“Tisanayambe ligi, tinakahala pansi ndi amnzathu yimbira masewero a mpira wamiyendo ndicholinga chowunikira mavuto zomwe analipi mmbuyomu ndikupeza njira zothanirana nawo ndipo ndinene pano pokondwa kuti chaka chino sipakhala madando okhudza oyimbira kamba koti zonse zili mchimake,” anatsindika moteromo Kumwenda.

Mlembiyu anathokoza banki ya First Capital popitiliza kuthandiza ligiyi ndi ndalama.

“Ichi ndichyambi chotukula mpira wamiyendo mdziko muno. Anawa ndiomwe adzatumikire matimu osiyanasiyana m’dzikomuno komanso timu ya dzikolino. Kutero ndiwathokoze a First Capital Bank popitiliza kuthandiza. Kuthokoza kwakukulu ndikoti tionetsetsa ngati komiti kuti matimu akhale osunga mwambo ndipo ngati pangapezeke timu yophwanya malamulo oyendetsera ligi yathuyi, malamulo adzagwira ntchito mosayang’ana nkhope. Ndikuwafunira matimu zabwino zonse ndipo akhale olimbikira,” anatero Kumwenda.

Mmasewero omwe aseweredwa musabata yoyamba, timu ya Sanwecka inagonjetsa timu  ya Mbahewe ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi ndipo Prince Njaliwa ndi Chancy Kawonga anagoletsera timu ya Sanwecka pamene Ben Mangani anapezera chigoli chachipukuta misonzi timu yake ya Mbahewe.

Pamasewero ena, timu ya  Topik Academy (a katswiri omwe akuteteza ligiyi) inayamba udyo masewero ake kamba koti inasambitsidwa chokweza ndi  timu ya Chipilingu ponwe inagonja ndi zigoli ziwiri kwa duu. Worship Bwazi wa Topik Academy anawonetsetsa kuti asangotuluka m’bwalo la zamasewero popanda kugwedeza ukonde chifukwa anakwanitsa kugoletsa chigoli chimodzi pamene Yewo Nyirenda ndi Lameck Chavula anamwetsa aliyense chigoli chimodzichimodzi zomwe zinapezetsa chipambano timu ya Chipilingu.

Masewero onsewa anaseweredwa pabwalo la Chiwavi Primary School ground mummzinda wa Mzuzu.

Matimu khumi ndi anayi ndiomwe akhale akuchotsana chimbenene muligiyi.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Nyamilandu Hails the Flames

Nyamilandu Hails the Flames

Hands Off the Stadium Issue.

Hands off the stadium issue

HRDC Stand on Stadium Construction Ignites Hot Debate

HRDC Stand on Stadium Construction Ignites Hot Debate

error

Share Breaking News