Home » News » Nyumba Ya Malamulo Ayitsegulira Pa 21Juni

Nyumba Ya Malamulo Ayitsegulira Pa 21Juni

Spread the love

Leo Mkhuwala

Nyumba ya malamulo yomwe aphungu ake akhale akupanga malamulo m’zaka zisanu za kutsogoloku ayitsegulira Lachisanu sabata ya mawa pa 21 Juni.

M’kalata yake polengeza izi, kalaliki wa nyumbayi, Mayi Fiona Kalemba wapempha aphungu onse omwe angosankhidwa kumene kuti patsikuli, adzapezeke atafika m’nyumba ya malamulo nthawi ikadzamati 10 koloko m’mawa.

“Aphungu onse akupemphedwa kudzakhala nawo pa nkhumanowu pa nthawi komanso malo omwe tawapatsa mpaka pomwe nyumbayi idzamalize zokambirana,” watero Kalemba m’kalatayo.

M’kalatayi, kalalikiyu wapemphanso alendo onse oitanidwa kuti adzakhale m’mipando mwawo nthawi ikadzamati 8:30 m’mawa.

Nkhumanowu womwe ndi wa nambala 48 uchitike kwa sabata zitatu kuyambira pa 21 Juni mpaka pa 12 Julaye.

Pulezidenti wa dziko lino, Arthur Peter Mutharika ndi yemwe adzatsegulire nkhumanowu.

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Thank you Malawians for voting me again- Mutharika

Thank you Malawians for voting me again- Mutharika

NATIONAL ADDRESS BY RIGHT HON. DR. LAZARUS CHAKWERA,

PRESIDENT OF MALAWI CONGRESS PARTY, DELIVERED AT MCP HEADQUARTERS IN LILONGWE. SATURDAY, JUNE 8, 2019

SABC CHIEF AUDIT EXECUTIVE SURVIVES ASSASSINATION ATTEMPT

SABC CHIEF AUDIT EXECUTIVE SURVIVES ASSASSINATION ATTEMPT