Home » News » Amayi Akhetsa Misonzi Kulilira Jane Ansah, Akonza Ulendo Wa Ndawala Kuonetsa Kukwiya

Amayi Akhetsa Misonzi Kulilira Jane Ansah, Akonza Ulendo Wa Ndawala Kuonetsa Kukwiya

Mtolankhani Wathu

Amayi Akhetsa Misonzi Kulilira Jane Ansah, Akonza Ulendo Wa Ndawala Kuonetsa Kukwiya

Gulu la amayi lomwe likudzitcha kuti “Forum For Concerned Women” motsogozedwa ndi Unduna woona za kusasiyana pakati pa amayi ndi abambo lati, wapampando wa bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), a Jane Ansah, sadalakwitse chirichonse pa nthawi ya chisankho chipitacho ndipo kuti pachifukwachi, sakuyenera kutula pansi udindo wawo monga momwe anthu ena akufunira.

Poyankhulira gululi Lolemba pamsonkhano wa atolankhani, Nduna Yoona kusasiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Mary Navicha komanso m’modzi wa amayi omwe amaona za malamulo, a Seodi White anadzudzula a mabungwe omenyera ufulu wa anthu komanso azipani zotsutsa boma ponena kuti, zomwe akuchita ponyazitsa Mayi Ansah, ziri m’gawo la nkhanza ndipo kuti anthuwa akuchita nkhanza zimenezi kamba koti Mayi Ansah ndi mzimayi.

Poyankhula kwinaku akukhetsa misonzi, a Navicha komanso a White anati iwo ngati amayi okhuzidwa salola kuti mayi mzawo apitilire kunyozedwa.

Pa mfundoyi, amayiwa analengeza kuti akonza ulendo wa ndawala womwe uchitike Lachitatu mu mzinda wa Blantyre pofuna kuonetsa kusakondwa kwawo ndi nkhanza zomwe mayi Ansah akuchitiridwa.

Ena mwa amayi odziwika bwino omwe anali nawo pa msonkhanowo ndi Mlembi Wamkulu m’chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), a Grizeldar Jeffrey, yemwe anali wachiwiri kwa Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, a Esther Mcheka Chilenje komanso Nduna yakale yoona za kusasiyana pakati pa Amayi ndi Abambo, a Cecelia Chazama.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

BOLA-CEFO Condemns Msundwe Protestors For Killing Police Officer

BOLA- CEFO CONDEMNS MSUNDWE PROTESTERS FOR KILLING POLICE OFFICER

Dowa To Fly MACOHA National Flag Week

DOWA TO FLY MACOHA NATIONAL FLAG WEEK

Strides Towards Peace, Reconciliation, Earns Ethiopian Prime Minister Nobel Prize

Strides Towards Peace, Reconciliation, Earns Ethiopian Prime Minister Nobel Prize

error

Share Breaking News