Home » Politics » Ochita Zionetsero Ku Lilongwe Amenya Ndi Kuvula Mzimayi Wapolisi Yemwe Akuti Amapanga Ukazitape

Ochita Zionetsero Ku Lilongwe Amenya Ndi Kuvula Mzimayi Wapolisi Yemwe Akuti Amapanga Ukazitape

Mtolankhani Wanthu

Ochita Zionetsero Ku Lilongwe Amenya Ndi Kuvula Mzimayi Wapolisi Yemwe Akuti Amapanga Ukazitape

Mkwiyo mu chipwirikiti chomwe Lachiwiri pa 6 Ogasiti chinabuka pakati pa anthu ochita zionetsero ndi apolisi mu mzinda wa Lilongwe unakhuthukila pa mayi wina wapolisi yemwe anapezeka ali nawo m’gulu la anthu ochita zionetsero akutola zithunzi zomwe anthu amaganiza kuti akufuna kukadzigwiritsa ntchito pa ukazitape.

Anthu omwe anamudzindikira mayiyu anamemeza anzawo ndipo posakhalitsa, wapolisiyo anapezeka ali m’manjam’manja mwa anthu okwiya.

Mu kanthawi kochepa, anthu anayamba kumumenya wapolisiyo kwinaku akumuvula nkumusiya ali mawere pa mtunda komanso zovala zamkati zikuoneka.

Pakadali pano, anthu osiyanasiyana omenyera ufulu wa amayi ayambapo kudzudzula ponena kuti mchitidwe wovula amayi ngosavomerezeka m’bwadwo uno wamakono kamba koti kutero kumanyazitsa komanso kuchotsa ulemu wa amayi.

Kumayambiliro a chaka chino, mchitidwe wonga uwu udachitika kwa M’baluku m’boma la Mangochi pamene anthu ena omwe amawaganizira kuti amatsatira chipani cha DPP adavula mayi yemwe ndi m’modzi wa akuluakulu a chipani cha UTM m’bomalo.

Pakadali pano, wofalitsa nkhani ku likulu la apolisi ku Lilongwe, a James Kadadzera sadanenepo kanthu pa chirichonse chokhuza zionetsero koma wati posachedwapa apolisi ayankhulapo.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Just In; PAC Meeeting Mutharika To Discuss Post Election Political Impasse

Just In; PAC Meeeting Mutharika To Discuss Post Election Political Impasse

MAENGA faults Government on UN Propaganda

MAENGA FAULTS GOVERNMENT ON UN PROPAGANDA

MEC resumes collection of sworn in statements

MEC RESSUMES COLLECTION OF SWORN STATEMENTS

error

Share Breaking News