Home » National » Wansembe, Malemu Bambo Dasiano Muhime Alowa M’manda Lachinayi

Wansembe, Malemu Bambo Dasiano Muhime Alowa M’manda Lachinayi

Mtolankhani Wathu

Wansembe, Malemu Bambo Dasiano Muhime Alowa M’manda Lachinayi

Wamsembe wa mpingo wa Katolika yemwe wamwalira masana wa Lachiwiri mu Arilidayosisi ya Blantyre, malemu Bambo Dasiano Muhime ayikidwa m’manda Lachinayi pa 8 Ogasiti, 2019.

Malinga ndi dongosolo la maliro lomwe akulikulu la mpingowu atulutsa, mwambo udzayamba nthawi ya 10 koloko m’mawa ndi nsembe ya Misa mu tchalichi cha Limbe Cathedral ndipo mapempherowa adzatsogolere ndi mkulu wa ansembe mu arikidayosisi ya Blantyre, Ambuye Episikopi Thomas Luke Msusa.

Thupi la malemu Bambo Muhime adzaliyika m’manda a Limbe Cathedral pambuyo pa nsembe ya Misa.

Dongosolo la maliro likukambanso kuti thupi la malemu Bambo Muhime alinyamula kuchoka nalo ku nyumba yachisoni ya sukulu yosula madotolo ya College of Medicine Lachitatu nthawi ya 3 koloko masana.

Dongosolo likufotokozanso kuti mwambo woyamba wa nsembe ya Misa uchitika masana a Lachitatu kuyambira nthawi ya 5 koloko mtchalitchi lomweli la Limbe Cathedral.

Bambo Muhime omwe amwalira pa chipatala Adventist mu mzinda wa Blantyre adawadzodza unsembe m’chaka cha 1969 ndipo atumikira Mulungu kwa zaka pafufupi makumi asanu (50).

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Agriculture Ps urges Journalists to love Malawi

AGRICULTURE PS URGES JOURNALISTS TO LOVE MALAWI

MCP Want PSLC Results Suspended, Press MANEB To Explain Selection Criteria Used

MCP Want PSLC Results Suspended, Press MANEB To Explain Selection Criteria Used

BREAKING NEWS!Petrol Bombed: MCP Vice President, Sidik Mia’s Office Burnt In The Wee Hours Of Night

Petrol Bombed: MCP Vice President, Sidik Mia's Office Burnt In The Wee Hours Of Night

error

Share Breaking News