Home » National » Mulowa M’malo Wa Mfumu Yaikulu Ya Alhomwe Amusankha Pambuyo Pa Miyezi Iwiri

Mulowa M’malo Wa Mfumu Yaikulu Ya Alhomwe Amusankha Pambuyo Pa Miyezi Iwiri

Mtolankhani Wathu

Mulowa M’malo Wa Mfumu Yaikulu Ya Alhomwe Amusankha Pambuyo Pa Miyezi Iwiri

Bungwe lomwe limalimbikitsa miyambo ndi chikhalidwe cha mtundu wa Alhomwe, la Mulhakho wa Alhomwe lati mfumu yatsopano yomwe ilowe m’malo a malemu mfumu yaikulu Ngolongoliwa ayisankha mmiyezi iwiri ikudzayi.

M’modzi wa akuluakulu ku bungweli, Mchana Mkwaye Mpuluka wauza atolankhani kuti ndondomeko yosankha mfumu yatsopano ichitike kumapeto kwa mwezi ukubwerawu Seputembala kamba koti panthawiyo nyengo yolira maliro a Mfumu Ngolongoliwa idzakhala itafika kumapeto.

Mkuluyu ananenanso kuti panthawiyo, dongosolo losankha mfumu yatsopano lidzayamba ndi nkhumano ya mafumu a mtundu wa Chilhomwe omwe adzasankhe mlowa m’malo ndipo yemwe adzavomereze dzina la mfumu yatsopano ndi mkulu woyang’anila bungweli yemwe ndi Pulezidenti Peter Mutharika.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Police arrests two for conduct on a police officer

POLICE ARRESTS TWO FOR CONDUCT ON A POLICE OFFICER

Agriculture Ps urges Journalists to love Malawi

AGRICULTURE PS URGES JOURNALISTS TO LOVE MALAWI

MCP Want PSLC Results Suspended, Press MANEB To Explain Selection Criteria Used

MCP Want PSLC Results Suspended, Press MANEB To Explain Selection Criteria Used

error

Share Breaking News