Home » National » A Mutharika Akuwafuna Ku Bwalo La Milandu

A Mutharika Akuwafuna Ku Bwalo La Milandu

Mtolankhani Wathu

A Mutharika Akuwafuna Ku Bwalo La Milandu

Patongotha masiku awiri mlandu wokhuza chisankho cha Pulezidenti utalowa m’khothi, maloya a chipani cha Kongeresi ati akufuna a Peter Mutharika omwe ndi mtsogoleri wa dziko lino abwere ku khothi kudzaperekera umboni.

M’modzi wa maloya a mtsogoleri wa chipani cha Kongeresi, a Titus Mvalo, wati a Mutharika akuyenera kufika ku bwalo lamilandu kuti adzayankhe mafunso omwe chipanichi chakonzeka kudzawafunsa.

Pa mlandu wa chisankho womwe uli m’bwalo lowona za malamulo mu mzinda wa Lilongwe, Presidenti Mutharika pamodzi ndi bungwe lowona za chisankho akufuna kuti bwalo lithetse mlandu womwe atsogoleri a zipani za Kongeresi ndi UTM adakadandaula ku bwalo lamilandu.

A Mutharika kudzera mwa owaimila akuti umboni womwe a Chakwera ndi a Chilima ali nawo ngosayenera kamba koti awiriwa akufuna bwalo linene kuti zotsatila za chisankho za pulezidenti nzopanda ntchito kamba koti a bungwe la zachisankho adagwiritsa ntchito zofufutira zilembo zotchedwa “Tipp-ex”.

Bungwe la zachisankho lidalengeza kuti a Mutharika ndi omwe adapambana chisankho ndi mavoti 1, 940, 709 ndipo kuti wotsatira adali mtsogoleri wa Kongeresi, a Lazarus Chakwera ndi mavoti 1, 781, 740 ndipo wachitatu adali mtsogoleri wa UTM, a Saulos Chilima omwe akuti adapeza mavoti 1, 018, 369.

Bwalo lamilandu lidamanga mtolo umodzi madandaulo a Chakwera ndi a Chilima ndipo lidakhadzikitsa ma Jaji asanu kuti amve mlanduwu.

Mlanduwu udayamba Lachinayi lapitali ndipo udalowanso Lachisanu pamene mtsogoleri wa UTM amayankha mafunso kuchokera kwa mkulu woimila boma pa milandu, a Kalekeni Kaphale.

Mlanduwu womwe akhale akuumva kwa masiku khumi ndi awiri (12) ulowanso m’bwalo la milandu Lolemba lino.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Malawi Develop Response Plan For Ebola

Pic: Dowa District Health Promotion Officer ( DHPO) Davie Nuka....health workers have been trained in infection prevention and case management.

Son Kills Mother In Chitipa

Son Kills Mother In Chitipa

Child Rights Organization Appeal for Support

Child Rights Organization Appeal for Support

error

Share Breaking News