Home » Uncategorized » Apolisi Agwira Mamuna Kamba Kowona Maliseche A Mayi Ake Omubereka

Apolisi Agwira Mamuna Kamba Kowona Maliseche A Mayi Ake Omubereka

Mtolankhani Wathu

Apolisi Agwira Mamuna Kamba Kowona Maliseche A Mayi Ake Omubereka

Mamuna wa zaka 26 zakubadwa, m’boma la Mchinji, Richard Bwanali ali m’manja mwa apolisi kamba kowona maliseche a mayi wake womubereka.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, Kaitano Lubrino wauza Malawi Freedom Network kuti pa 8 Ogasiti, Bwanali adalowa ku bafa komwe mayi wake amasamba nkumawaonela maliseche.

Mayiyu yemwe ali zaka 48 zakubadwa akuti adadzidzimuka ataona mwana wawo ataima potero ndipo adamufunsa chomwe amafuna koma mwana wawoyo sadayankhe ndipo adangopitilira kuyang’ana maliseche a mayiwo.

Chifukwa cha mantha, mayiyo adapfuula kupempha anthu kuti amuthandize.

Atamva kuti achibale akufuna kumufunsa kuti afotokoze chomwe amafuna pomakaona maliseche a mayi ake, Bwanali adathawa kufikila tsiku lotsatira pamene apolisi adamugwira.

Malinga ndi Kaitano, pakadali pano, apolisi apeza mlandu wopanga zinthu zomwe zingadzetse mpungwepungwe womwe amutsegulira woganiziridwayu.

Zadziwikanso kuti woganiziridwayu adagwirapo ukaidi woba njinga ya kapalasa ndipo waturuka ku ndende kumayambiliro a chaka chino.

Woganiziridwayu, amachokera m’mudzi wa Robert, Mfumu yaikulu Zulu, m’boma la Mchinji.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

MAENGA WARNS AUTHORITIES OF MALAWI CIVIL WAR

By: Vincent Gunde The Malawi Engagement Group ( MAENGA), an Utopian Philosophy ...

MCP Veep Sidik Mia Joins In Blantyre Peaceful Demos

MCP Veep Sidik Mia Joins In Blantyre Peaceful Demos

Demonstrators In Lilongwe Chase Suspected DPP Cadets On Spying Mission: Whisked Away By Police

Demonstrators In Lilongwe Chase Suspected DPP Cadets On Spying Mission: Whisked Away By Police

error

Share Breaking News