Home » Business » Dziko Lingapindule Pa Chuma Pokopa Alendo Kudzaona Miyambo Ndi Chikhalidwe, Yatero Nduna, Mary Navicha Ku Mdawaku Wa Atonga

Dziko Lingapindule Pa Chuma Pokopa Alendo Kudzaona Miyambo Ndi Chikhalidwe, Yatero Nduna, Mary Navicha Ku Mdawaku Wa Atonga

Mtolankhani Wathu

Dziko Lingapindule Pa Chuma Pokopa Alendo Kudzaona Miyambo Ndi Chikhalidwe, Yatero Nduna, Mary Navicha Ku Mdawaku Wa Atonga

Boma kudzera mwa nduna yomwe inaimila mtsogoleri wa dziko lino ku nkhumano wokumbukira miyambo ndi chikhalidwe cha Atonga, a Mary Thom Navicha, wati dziko la Malawi lingapindule pa chuma kudzera mu zikondwelero za miyambo ndi chikhalidwe cha mitundu yosiyanasiyana.

Ndunayi, yomwenso inali mlendo wolemekezeka ku mwambowu womwe unachitika Loweruka ku Mkondezi m’boma la Nkhatabay, inati tsopano boma liri ndi chidwi chopanga zikondwelero zamtunduwu kukhala imodzi mwa ntchito zokopa alendo, ponena kuti, maiko ena monga dziko la Aeguputo lakwanitsa kuchita izi.

Hon Mary Navicha

“Ndikukhulupilira kwambiri kuti dziko la Malawi lingakwere pa chuma kudzera mu ntchito yotukula chikhalidwe ndi miyambo,” anatsimikiza motero a Navicha omwenso ndi nduna yoona za kusasiyana pa kagwiridwe ka ntchito pakati pa amayi ndi abambo.

Iwo anati ndi okondwa kuti pakadali pano anthu amitundu yosiyanasiyana m’dziko muno ali pa kalikiliki kuonetsetsa kuti miyambo ndi zikhalidwe zawo zisataike.

Pamfundoyi, ndunayi inapempha mabungwe onse a chikhalidwe ndi miyambo kuti atengepo gawo pa ntchito yokhadzikikitsa mabungwe kuti afike pa mlingo wovomerezeka ndi kukhala nako kuthekera komakopa alendo.

A Navicha anatsindikanso mfundo ya kufunika koti, anthu a mitundu yosiyanasiyana adzikhalirana mwa mtendere ndipo ananenetsa kuti, zikondwelero zolimbikitsa chikhalidwe ndi miyambo zikuyenera kukhala chida cholimbikitsa umodzi wotere.

Ndunayi inati m’nyengo ya makono, mchitidwe wosankhana mitundu kapena zigawo zochokera sukuyenera kupatsidwa mpata pakati pa Amalawi.

Pamwambowu panalinso akulu-akulu osiyanasiyana, monga wapampando wa bungwe la Mdawaku wa Atonga, Professor John Kalenga Saka yemwe anati, mu zaka zisanu (5)zikudzazi, bungweli lakonza zochirimika pa ntchito yopititsa patsogolo ntchito za bungweli maka ku mbali ya zachuma.

Pakadali pano, mitundu monga ya Alhomwe, Angoni, Atumbuka, Atonga, Ayawo komanso Achewa ndi yomwe yakangalika pa ntchito yokhadzikitsa mabungwe a miyambo ndi chikhalidwe.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Nyamilandu Hails the Flames

Nyamilandu Hails the Flames

Hands Off the Stadium Issue.

Hands off the stadium issue

Malawi Government Peggs The 2019/2020 National Budget At K1.7 Trillion…Minimum Wage Adjusted Upwards

Malawi Government Peggs The 2019/2020 National Budget At K1.7 Trillion…Minimum Wage Adjusted Upwards

error

Share Breaking News