Home » Latest » Anthu 7 Afa Pangozi M’boma La Ntcheu

Anthu 7 Afa Pangozi M’boma La Ntcheu

Mtolankhani Wathu

Anthu 7 Afa Pangozi M’boma La Ntcheu

Malipoti ochokera m’boma la Ntcheu atsimikiza kuti anthu asanu ndi awiri (7) afa pangozi ya pamsewu yomwe yachitika m’mawa wa Lachinayi m’boma la Ntcheu.

Ngoziyo yachitikira pamalo otchedwa Kanyimbo m’bomalo pamene lole yaikulu yomwe nambala yake ndi NA 4075 idasempha msewu ndi kuomba galimoto zina kuphatikizapo minibasi yomwe inanyamula anthu.

Loleyo yomwe imachokera ku Dedza kulowera ku Ntcheu, inanyamula mabelo a fodya ndipo anthu omwe anaona ngoziyo ikuchitika akuti loleyo imathanga kwambiri kufikira pomwe inasiya msewu kamba koti dalaivala analephera kuongolera komanso kuimitsa.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Ntcheu, a Hastings Chigaru, anthu 7 amwalira ndipo ena atatu (3) avulala modetsa nkhawa.

Chigaru wati anthu omwe avulala awagonetsa pa chipatala cha boma ku Ntcheu komwe akulandira thandizo la mankhwala.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

UTM Witness Alleges President Mutharika Was Advantaged By Electoral Process

UTM Witness Alleges President Mutharika Was Advantaged By Electoral Process

Malawi Government Peggs The 2019/2020 National Budget At K1.7 Trillion…Minimum Wage Adjusted Upwards

Malawi Government Peggs The 2019/2020 National Budget At K1.7 Trillion…Minimum Wage Adjusted Upwards

HRDC Stand on Stadium Construction Ignites Hot Debate

HRDC Stand on Stadium Construction Ignites Hot Debate

error

Share Breaking News