Home » Uncategorized » Bwalo Lamilandu Lati Mlandu Wachisankho Udzapitilira Pa 3 September

Bwalo Lamilandu Lati Mlandu Wachisankho Udzapitilira Pa 3 September

Wolemba: Leo Mkhuwala

Bwalo Lamilandu Lati Mlandu Wachisankho Udzapitilira Pa 3 September

Khothi la zamalamulo mu mzinda wa Lilongwe lati lidzapitilira kumva mlandu wa zotsatira za chisankho cha Pulezidenti pa 3 Seputembala lomwe ndi Lachiwiri sabata la nkuja.

Bwalo lisanaimitse mlanduwu Lachisanu, woweruza yemwe akutsogolera pokumva mlanduwu, a Healey Potani, anati pakadali pano bwalo silingamve pempho lomwe bungwe la zachisankho la Malawi Electral Commission (MEC) kudzera mwa maloya ake lapereka loti abweretse m’mbwaloli umboni wina wapadera wa mau ojambulidwa.

Jaji Potani wati bwalo lidzapereka mpata mtsogolomu wokumva pempholi.

Bwaloli linakananso pempho la maloya a Pulezidenti Peter Mutharika loti lifunse mafunso mboni zokwana 243.

Bwalo lakana pempholi ponena kuti maloya oyimila Pulezidenti Mutharika sadaonetse chenicheni chomwe akufuna mu pempho lawolo.

Mlandu Lachisanu unayamba mochedwa kamba koti maloya a mbali zonse zokhudzidwa sanabweretse ndondomeko ya mboni.

Pa mlanduwu, chipani cha Kongeresi chiri ndi mboni khumi ndi zisanu (15), bungwe la MEC mboni makumi anayi ndi mphambu zitatu (43) ndipo mboni za a Mutharika zilipo mazana awiri, makumi anayi ndi mphambu zitatu (243).

M’sabatayi, maloya oyimila bungwe la MEC anakangalika kufunsa mafunso a Mirriam Gwalidi omwe ndi mboni ya wodandaula woyamba, a Saulos Klaus Chilima omwe ndi pulezidenti wa chipani cha UTM.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

MEC Junior Staff Plan Strike Against Bosses Allowance Scam

MEC Junior Staff Plan Strike Against Bosses Allowance Scam

Maenga response to IG of Malawi Police Service Rodney Jose

MAENGA RESPONSE TO INSPECTOR GENERAL OF MALAWI SERVICE RODNEY JOSE IN CALLING ...

Muluzi Meets Mutharika Over Jane Ansah

Muluzi Meets Mutharika Over Jane Ansah

error

Share Breaking News