Home » Latest » Pa Mlandu Wokhuza Chisankho Ku Mangochi Monkeybay, Bwalo Lakana Pempho La A Ralph Jooma Loti Mlandu Authetse

Pa Mlandu Wokhuza Chisankho Ku Mangochi Monkeybay, Bwalo Lakana Pempho La A Ralph Jooma Loti Mlandu Authetse

Mtolankhani Wathu

Pa Mlandu Wokhuza Chisankho Ku Mangochi Monkeybay, Bwalo Lakana Pempho La A Ralph Jooma Loti Mlandu Authetse

Bwalo la milandu la High Court mu mzinda wa Blantyre lakana pempho la oyankha mlandu wachiwiri, a Ralph Jooma loti mlandu wokhuza chisankho cha phungu m’dera la Mangochi Monkeybay womwe pakadali pano uli m’bwalo la milandu authetse.

Bwalo lakana pempholi Lachisanu lapitali pa 29 Ogasiti pamene limamva mapempho atatu (3) kuchokera ku mbali ya odandaula, a Gerald Kazembe a chipani cha Malawi Congress ndi omwe akuyankha mlanduwu achiwiri, a Ralph Jooma.

Pa mapemphowa, odandaula anapereka pempho limodzi pamene oyankha mlandu achiwiri anapereka mapempho awiri.

Mu pempho lawo loyamba lomwe bwalo lakana, maloya omwe akuimila a Ralph Jooma amafuna kuti bwalo lithetse mlandu ati kamba koti pali zolakwika zina ndi zina zokhudza mlanduwu.

Mu pempho lachiwiri, maloya a Ralph Jooma akufuna kuti bwalo liitane mboni kudzayankha mafunso pa maumboni a zikalata zomwe akuzitcha GK11 (a) ndi GK11 (b).

Mu pempho lachitatu, maloya omwe akuimila a Gerald Kazembe akuima nji! pa pempho lawo lomwe akufuna m’modzi wa akulu-akulu ku bungwe lowona za chisankho la Malawi Electral Commission (MEC) afike ku bwalo lamilandu kudzayankha mafunso.

Pa pempho lachiwiri, a Kamkwasi omwe ndi loya wa a Jooma anabwelera m’mbuyo ndi ganizo loitanitsa mboni kuti kickstand mafunso pa zikalata zomwe zinatanthauza kuti atsale ndi pempho limodzi lofuna kuthetsa mlandu lomwe bwalo linakana.

Ku mbali ya odandaula, bwalo linauza maloya omwe akuimila a Kazembe kuti akonze zina ndi zina zina zokhuza pempho lawo pa mlanduwu kuti potero zithandize bwalo kumva komanso kutsatira mlanduwu mosavuta.

Dzadziwikanso tsopano kuti yemwe akudandaula pa mlanduwu, a Gerald Kazembe awonjezera maloya ena awiri, a Justin Dzonzi ndi a Henry Ngutwe maloya otchuka comwe akhale akuwaimila pa mlanduwu.

Masiku a m’mbuyomu pamene mlanduwu unkayamba, a Kazembe amaimiridwa ndi m’modzi mwa maloya otchuka m’dziko muno, a Patrick Maliwa.

Pa mlanduwu omwe bungwe la MEC pamodzi ndi a Ralph Jooma akuyankha, wodandaula a Gerald Kazembe akufuna kuti bwalo linene kuti zotsatira za chisankho cha phungu chomwe chidachitika pa 21 May chaka chino m’dera la Mangochi Monkeybay, zomwe bungwe la MEC lidalengeza nzopanda ntchito.

A Kazembe akumenyetsa khwangwa pa mwala kuti iwo ndi omwe adapambana pa chisankhochi ngati phungu wa deralo ndipo kuti pa chisankhochi, padachitika za chinyengo zochuruka zomwe bungwe la MEC lidadzilekelera zomwenso zidapangitsa bungweli kulengedza kuti a Ralph Jooma achipani cha DPP ndi omwe adapambana.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

Mutharika, The Malawi President Goes To Town

Mutharika, The Malawi President Goes To Town

Pope Francis Arrives In Mozambique

Pope Francis Arrives In Mozambique

Communities Worries Over Government Priorities

Communities Worries Over Government Priorities

error

Share Breaking News