Home » Politics » Chipani Cha MCP Chikuti Nzochititsa Manyazi Kuti A Mutharika Adzipitilirabe Kunamiza Amalawi Pa Za Doko La Nsanje

Chipani Cha MCP Chikuti Nzochititsa Manyazi Kuti A Mutharika Adzipitilirabe Kunamiza Amalawi Pa Za Doko La Nsanje

Malawi Freedom Network

Chipani Cha MCP Chikuti Nzochititsa Manyazi Kuti A Mutharika Adzipitilirabe Kunamiza Amalawi Pa Za Doko La Nsanje

Mtsogoleri wa dziko kumapitilirabe kunamiza Amalawi maka anthu a m’boma la Nsanje kuti chitukuko cha doko la Nsanje nchotheka ndi zochititsa manyazi komanso zopatsa phwete, watero mkulu woona zokopa anthu m’chipani cha Kongeresi, a Moses Kumkuyu.

Kumkuyu amayankhula izi Lachisanu kwa Tengani m’boma la Nsanje pothilira ndemanga za ulendo wa a Peter Mutharika m’bomalo masiku apitawo pamene anafika ku doko la Nsanje ndikulonjeza anthu kuti boma lake liwonetsetsa kuti dokoli layamba kugwira ntchito monga mwachikonzero.

A Mutharika adauza anthu kuti chomwe boma likudikila ndi kumva kuchokera ku boma la dziko la Mozambique lomwe lidatenga udindo wopanga kauniuni pa za kuthekera koti dokoli liyambe kugwira ntchito.

Koma pokambapo mopanda kupsyatira mau, Kumkuyu wati nzotayitsa nthawi kwa anthu a m’boma la Nsanje kumamva malonjezo a bodza kuchokera kwa munthu yemwe akudzitcha mtsogoleri wa dziko pa nkhani ya chitukuko chachikulu ngati doko chomwe kwa nthawi yaitali tsopano anthu m’bomali akhala akuyembekedzera.

“Nzopatsa phwete kumamva bodza lotere kwa munthu yemwe akuti ndi mtsogoleri wa dziko chifukwa aliyense akudziwa kuti malo omwe akuwatcha doko tsopano adasanduka malo owailika omwe ndi bwinja la chionekere pomwe sitima angakhale bwato silingafike, iri ndi bodza lankungunidza lomwe tsopano lasanduka bodza lotopetsa,” anayankhula motero Kumkuyu.

Popitilira m’mau ake, Kumkuyu anadzudzula chipani cha DPP kamba ka mchitidwe wogawa chimanga ndi nandolo kwa anthu m’maboma a Nsanje ndi Chikwawa pa nthawi yomwe a Mutharika amafika pa ulendowu womwe cholinga chake adati nkudzayendera ntchito za chitukuko.

Kumkuyu ananenetsa kolimba kuti kugawa chimanga ndi nandolo si ntchito ya chitukuko ndipo kuti kutero nkungolimbikitsa chabe umphawi womwe pa nthawi ya ulamuliro wake, boma la DPP laudzala maka pakati pa anthu m’dziko muno.

“Iwowa a DPP ndi omwe akoledzera umphawi kuti chaka ndi chaka anthu azivutika ndi njala ndi cholinga choti adziwapatsa kachimanga komwe nkosakwanira pongofuna chabe kupezapo thamo pa ndale nkumaoneka ngati boma lothandiza,” anatero Kumkuyu.

Sabata lapitalo, Pulezidenti Mutharika adakonza ulendo wadzidzidzi wopita ku chigwa cha mtsinje wa Shire womwe adaukonza pambuyo pokumva kuti chipani cha MCP motsogozedwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri m’chipanichi, Sidik Mia amapita ku chigwachi kukachititsa msonkhano wothokoza anthu kamba kotenga nawo mbali pa chisankho chomwe chomwe chidalipo pa 21 Meyi.

Zodabwitsa zidali pomwe ofesi ya pulezidenti ndi nduna idaturutsa chikalata mmangummangu kulengeza kuti a Mutharika akupita ku chigwachi tsiku lomwe chipani cha MCP chinalengeza kuti chikukachititsa msonkhano.

Pa msonkhano wake pa bwalo la Mpatsa, chipani cha MCP chathokoza anthu mdera la pakati m’boma la Nsanje kamba koturuka mwaunyinji ndi kukaponya voti ndipo chapempha anthu kuti adikire mwa tcheru komanso mwachiyembekezo zotsatira za mlandu wa chisankho.

Pa msonkhanowu, chipanichi chatsimikizira anthu kuti malinga ndi zomwe chipanichi chidapeza komanso kalondolondo womwe akatswiri a DBO adachita, mtsogoleri wa MCP, Lazarus Chakwera ndi yemwe adapambana pa udindo wa pulezidenti pa chisankho chomwe chidalipo.

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

DPP Supporters Attack HRDC Leaders…Hack Activist Billy Mayaya…MCP Veep Sidik Mia Visit Him In Hospital

DPP Supporters Attack HRDC Leaders…Hack Activist Billy Mayaya…MCP Veep Sidik Mia Visit Him In Hospital

HRDC Leaders And UTM Veep Refuge At MDF Camp

Freelance Reporter HRDC Leaders And UTM Veep Refuge At MDF Camp HRDC ...

Ansah Resurface from Hiding

Ansah Resurface from Hiding

error

Share Breaking News