Home » Latest » Phungu M’boma La Nsanje, Francis Katsaila Asiya Kulipilira Sukulu Ana Ovutika Oposa 200

Phungu M’boma La Nsanje, Francis Katsaila Asiya Kulipilira Sukulu Ana Ovutika Oposa 200

Malawi Freedom Network Reporter

Phungu M’boma La Nsanje, Francis Katsaila Asiya Kulipilira Sukulu Ana Ovutika Oposa 200

Phungu woimila dera la pakati m’boma la Nsanje, Francis Katsaila wati wasiya kulipilira sukulu ana ovutika oposa mazana awiri (200) omwe amachokera m’derali.

Phunguyu yemwenso ndi nduna yoona nkhani za kunja kwa dziko lino ndi ubale wa dziko lino ndi maiko ena walengeza izi pamene anachititsa msonkhano mderali ndi cholinga chothokoza anthu omwe adamuvotera pa chisankho chomwe chinalipo pa 21 Meyi chaka chonchino.

Katsaila anafotokoza kuti ganizo loti asiye kulipilira anawa sukulu ladza pambuyo podzindikira kuti anawa pamodzi ndi makolo awo sadatenge nawo gawo lomuthandiza kuti apambane pa chisankhocho.

Iye anati walandira malipoti oti anawa pamodzi ndi makolo awo anali pambuyo pothandiza munthu yemwe ankalimbana naye pa chisankho, Kaffa Mandevana yemwe amaimila chipani cha Kongeresi.

Nkhani yokhuza kusamvana pa za kupambana pa chisankho kwa a Katsaila iri m’bwalo la milandu la High Court ndipo yemwe adakadandaula kubwaloli ndi a Mandevana omwe akumenyetsa khwangwa pamwala kuti iwo ndi omwe adapambana chisankho ndipo kuti a Katsaila adachita kubera mothandizana ndi bungwe lowona za chisankho la Malawi Electral Commission (MEC).

Malawi Freedom Network
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  
 •  

About malawi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

*

x

Check Also

GOVERNMENT PATIENCE AND TOLERANCE SHOULD NOT BE TAKEN FOR GRANTED

GOVERNMENT PATIENCE AND TOLERANCE SHOULD NOT BE TAKEN FOR GRANTED

Need to have permanent leader of opposition-Nankhumwa Calls.

Need to have permanent leader of opposition-Nankhumwa Calls.

“MCP Candidate Lazarus Chakwera Won The May 21 Presidential Elections”-Witness Tells Court

"MCP Candidate Lazarus Chakwera Won The May 21 Presidential Elections"-Witness Tells Court

error

Share Breaking News