Alezi apepha maphunziro ku Chikwawa.
Uncategorized
Wolemba: Grecium Gama.
Kusowekera kwa maphunziro kwa aphunzitsi amkomba phala m'boma la Chikwawa kukulowesa maphunzirowa pansi.
Izi zadziwika pamene bungwe la Community forum Organisation Limagawa mabuku komanso zoseweretsa ana ankomba phala m'sukulu za Chisomo Namabvu ndi Mulambe Community-Based Childcare Centre zomwe zikupezeka m'dera la mfumu yaikulu Mulilima komanso Katunga
Poyakhulapo mlangizi wochokera ku offisi yoona chisamaliro cha anthu bomalo , Lysan Mangasanja anati m'sukulu zambiri zikusowekera nthandizo la ndalama zogulira zithu monga mabuku komanso zithu zina zofunikira m'sukuluzo.
Iye anati aphunzitsi ambiri m'bomalo alibe lutso kapena upangiri wophunzitsira ana .
"Tipephe mabungwe komanso anthu akufuna kwabwino kuti abwere azaphunzitse aphuzitsiwa m'chol...