A Malawi Police amanga nurse wa chipatala cha Ntcheu District Hospital, a Chidawawa Mainje, a dzaka zakubadwa 39 powaganizira kuti ananyoza mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kudzera pa tsamba la mchezo la Whatsapp.
News update
Yapeza kuti a Mainje amachita mtsuso (debate) ndi anzawo pa whatsapp group. Mtsusowo unali wa ndale, okamba za momwe zinthu zikuyendera m’dziko muno mu ulamuliro wa Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake, Saulos Chilima.
Mtsusowo unakolera moto, ndipo Mainje anatemetsa nkhwangwa pa mwala kuti zinthu siziri bwino m’dziko muno, ndipo Chakwera walephera kuyendetsa dziko lino ngati mtsogoleri.
Ali mkati mwa mtsusowo, munthu wina pa group-yo anajambura (screenshot) zomwe anayankhura Mainje, ndipo adadziwitsa mkulu wina wa boma la Chakwera.
Mkuluyo atawona ma screenshot-wo anakwiya kwambiri, ndipo posakhalitsa galimoto ya police inabwera kuchokera komwe ku likulu la police ku area 30 mu mzinda wa Lilongwe, ndipo linamanga Mainje.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!