ACB Yamanga Anthu Asanu ndi atatu ogwira ntchito ku Immigration

Bungwe lothana ndi Katangale komanso ziphuphu la ACB lamanga anthu asanu ndi atatu ogwira ntchito ku nthambi yowona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno ndi anthu ena awiri kaamba kowaganizira kuti amachita za katangale pankhani yokhudza kupanga ziphanso zoyendera.

Malingana ndi kafukufuku yemwe bungwe la ACB linachita yapeza kuti anthu ena amapereka ndalama zokwana K200,000 pamwamba pa K50000 yomwe amayenera kupereka akamapangitsa chiphanso choyendera kapena kuti passport.

Ena mwa anthu oganizilidwawa akuti anapezeka ndi ndalama zankhaninkhani ndipo mmodzi wa iwo anapezeka ndi ndalama yokwana K2.5 million yomwe sanafotokoze bwino komwe yachoka.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *