
Wolemba: Myson Saidi, MULANJE
Bambo wina dzina lake Rex Kondwani, wadzikhweza m’boma la Thyolo atasemphana Chichewa ndi mkazi wake.
Chinatsitsa dzaye?
Mkaziyu akuti anakapereka ku kachisi wina ndalama yokwana K12 000 yomwe banjali linandira ngati malipiro litagwira ganyu yolima m’munda limodzi.
Apolisi akutinji?
Senior Superintendent George Kaleso ndi mkulu wa polisi ya Masambanjati ndipo akuti: “Mkaziyo adasunga ndalamazi. Dzulo, bambo Kondwani atapempha gawo lawo anawauza kuti ndalama zonse wapereka ku mpingo.”
Kusemphana Chichewa kunabuka!
Patapita kanthawi pang’ono, bamboyu, yemwe anali ndi zaka 45 zakubadwa, anapezeka atadzikweza ku denga la kachisi. Wadzipha!
Izitu zachitika m’mudzi mwa Muwalo, mfumu yaikulu Changata m’bomali.