
Olemba: Ambute Paimbe
Wachiwiri kwa Wachiwiri wa Sipikala wa Nyumba ya Malamulo yemwenso ndi Phungu wa nyumba ya Malamulo ku Nkungulu Olemekezeka Mai Aisha Mambo Adams lachinayi lapitalo anatsekukira msika omwe anthu amdera lake adzigulirako chimanga. Msikawu watsekukidwa pa Chimwala, mkuyankhula kwawo, Olemekezeka Aisha Mambo anapempha anthu amderali kuti asalore ma vendor kupangapo business koma awonetsetse kuti msikawu ukupindulira anthu amderali. Iwo anapemphanso atsogoleri amderali kutengapo gawo poonetsetsa kuti pamsikawo sipakuchitika chipolowe chilichonse komanso zachinyengo.
‘Ndipemphe anthu nonse kuti tigwirane manja pofuna kutukula dera lathu. Anthu ambiri amapeza mochepekedwa ndipo kubwera kwamsikawu kuwathandize anthu amenewo, zikatero chitukuko chidzapita patsogolo. Tisalore ma vendor kubwera kudzatitengera chimangachi ndipo tisapange chisokonezo pamsikapa chifukwa zikadzatero boma litha kudzasamutsa msikawu zomwe zidzapweteke anthu