
Wolemba: Rachael Julaye, LILONGWE
Kukula kwa mchitidwe ophana mwa chisawawa, umbava komanso ziwawa mdziko muno kwapangitsa gulu la abusa la Pastors Link komanso mzika zokhudzidwa kukonza mapemphero ofuna kuthana ndi ziwanda zomwe akuti zikukolezera zonsezi.
Mneneri wa omwe akonza mwambowu, Evangelist Stevie Chimwaza wati mapempherowa achitikira ku Robins Park Hall munzinda wa Blantyre Lolemba sabata ya mawa.
Chimwaza wati akufuna kubwera pa maso pa Mulungu pa zinthu zambiri zomwe zikupitilira kubala chisoni chochuluka pakati pa aMalawi.
Apa, iye wapempha aMalawi akufuna kwabwino kuti abwere mwaunyinji kudzakhala nawo pa mwambowu.
”Ndipemphe aMalawi asataye mtima kaamba koti Mulungu amamva komanso amayankha. Tili ndi chiyembekezo kuti mapempherowa tichita m’mizinda yonse ya mdziko muno.
“Koma pakadali pano, tipemphe anzathu a nyumba zoulutsa mawu kuti atithandize kuulutsa mwambowu kuti anthu onse athe kutenga nawo mbali,” watero Chimwaza.
Mapempherowa akudza kutsatira imfa zomwe zakhala zikuchitika mdziko muno maka ku Lilongwe komwe anthu anayi anaphedwa msabata imodzi.
Kuonjezera apo, mchitidwe wa umbanda ndi umbava wafika povuta kwambiri mdziko muno zomwe akatswiri ena olankhula pa zosiyanasiyana akuti zitha kugwirizana kwambiri ndi kusokonekera kwa chuma mdziko muno.
Masiku angapo apitawo, nduna yofalitsa nkhani Moses Kunkuyu idauza aMalawi kuti boma lichita chilichonse pofuna kuonetsetsa kuti chitetezo chili mchimake kuti anthu adzichita ntchito zawo mwa ufulu.
Iwo adatinso awonetsetsa kuti kafukufuku pa imfa za anthu omwe aphedwa masiku apitawa achitike bwino kuti aMalawi adziwe chilungamo.
Koma kumayambiliro, nduna ya za chitetezo, Ken Zikhale Ng’oma idakwiyitsa aMalawi komanso magulu omenyera ufulu pomwe idati kuphedwa kwa anthu atatu okha pa anthu 20 million sizikusonyeza kuti mdziko muno mulibe chitetezo.