Apolisi Siyani Nkhanza Kwa Nzika–Chakwera

President Lazarus Chakwera wamema apolisi m’dziko muno kuti apewe mchitidwe wa nkhanza ngati njira yothandizira kuthuzitsa mitima ya Amalawi pambuyo pa imfa zowirikiza zomwe zinachitika mwezi watha wa June.

Chakwera wapereka pempholi mu mzinda wa Lilongwe lero pamwambo wa mapemphero okumbukira zaka makumi asanu ndi limodzi – 60 za ufulu wodzilamulira ngati dziko.

Pamwambowo, opembedza anaperekanso ulemu ndi kupemphelera mizimu ya Vice President Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu omwe anafa pangozi ya ndege m’nkhalango ya Chikangawa pa 10 June.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *