
Oimbayu, yemwe amadziwika bwino ndi nyimbo zokhudza umoyo komanso chikhalidwe cha anthu, walandira chiyamiko pa nyimbo yake yatsopano yomwe akuitcha, “Nchape.”
Mu nyimboyi, Elias Missi, yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Atoht Manje, wayankhula motsutsana ndi mchitidwe wa nsanje omwe akuti ndi oononga.
Mkuluyu, yemwe mu kanema wa nyimboyi wagwilitsa ntchito anthu ovina chamba cha Beni, akudzudzula anthu omwe amapanga zinthu za ena.
Atoht Manje akuyimba kunena kuti, “Mphuno zawo zili bize kufwenkha… kufwenkha bizinezi zayeni, kufwenkha zomwe wawadalitsa mulungu,” apa oimbayu akungotsindika za momwe anthu akhalidwe amazipelekera akafuna kuchita za ena.
Iye akupitilira kunena kuti anthuwa ali ndi miyendo ya mphamvu yomwe imakhala ndi kuthekela kofika kulikonse komwe angakachite mjedo, kukambirana nkhani zokhudza anzawo.
“Miyendo yawo siitopa kuyenda, yakaliyakali anzanga kuyendako, kusaka ojeda nawo… kujeda nyengo za anzawo…” watero Atoht Manje.
Mu nyimboyi, Atoht Manje akuti anthu akhalidwe lotere akudwala ndipo akufunika mankhwala, ndipo mankhwalawa akutchula kuti “Nchape”.
Kuno ku Malawi, “Nchape” umadziwika ndi mbiri yotsuka mthupi.
Ndi chifukwa chake iye akuti anthuwa akuyenela kupatsidwa “Nchape,” kuti achile ku nthenda ya mjendo.
Izi zili mu kolasi ya nyimboyi momwe akuti, “Apatseni Nchape..Akumva kuwawa…Mwina Nchape uchotse nsanje mumtimamo… adziwe moyo simpikisano…”
Ngakhale nyimboyi ili ya chamba chachiMalawi (lokolo), zaonetsa kuti ili ndi chikoka kutengera ndi ndemanga zomwe zayankhulidwa pa nyimboyi.
Mwachidule, Atoht Manje mu nyimboyi akudzudzula khalidwe la mijedo lomwe akuti ndi loipa, lomwe malinga ndi iye, lakhazikika mmitima ya anthu mdziko muno.