Chisale Walandira Belo Amuletsa Kulankhula Ndi Atolankhani

1 min read

Wolemba: Robert Edward, LILONGWE

Bwalo la milandu ku Lilongwe tsopano latulutsa pa belo a Norman Chisale komatu awaletsa kulankhula ndi olemba nkhani mpakana mulandu wawo udzathe.

Principal Resident Magistrate Rodrick Michongwe wauzanso a Chisale kuti asamakonde kukwiya komanso kuti adzikaonekela ku likulu la apolisi Lachisanu lililonse m’mawa.

Kuonjezera apo, Michongwe walamula a Chisale kupereka chikole cha K500 000 komanso china chomwe ndalama zake zikukwana K1million.

Apolisi adamanga a Chisale Lachiwiri sabata yatha ati kamba kolankhula zonyoza komanso kuopseza anthu ena omwe akuyendetsa milandu yawo ina yomwe ili ku khothi pomwe ankalankhula ndi kanema wa Zodiak.

A Chisale, omwe adakhalapo wa chitetezo wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Peter Mutharika, adati nduna yoona za chilungamo a Titus Mvalo komanso mkulu wakale wozenga milandu ya boma a Steven Kayuni akuwazunza iwo ndi banja lawo.

Kum’mawaku, gulu la anthu linafika ku khothi kuperekeza a Chisale ndipo amaimba nyimbo zowatamanda.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours