Chitipa United, Ikusaka Mphunzitsi Wina

Timu ya Chitipa United yalowa pa msika kusakasaka mphunzitsi watsopano pamene yemwe amayitsogolera McNebert Kazuwa komanso omunthandizira Elvis Kafoteka asiya ntchito.

Malingana ndi mlembi wamkulu wa timu ya Chitipa a Watson Kabaghe, aphunzitsiwa asiya kaamba kakusachita bwino kwa timu.

A Kabaghe ati padakali pano Gift Nathaniel Mkamanga ndi Wachisa Mukhondia ndi omwe akhale ngati aphunzitsi ogwilizira.

Timu ya Chitipa United ili ndi ma point asanu amene yapeza m’masewero asanu ndi atatu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *