Civo yakana zowalirana mu chikho cha FDH

Polingalira thumba lomwe limapita kwa opambana mu mpikisano wa chikho cha FDH Bank, anyamata a m’boma a Civo masanawa avinitsa chindendelinde anyamata a Chihame All Stars ndi zigoli 5 kwa 1.

Powopa kuchitidwa chipongwe ndi anawa, Civo inamwetsa chigoli pa mphindi ten za chigawo choyamba kudzera mwa katswiri wawo, Righteous Banda.

Ndipo ichi chinali chiyambi cha mvumbi wa zigoli pomwe, Foster Biton anamwetsa zigoli ziwiri, Emmannuel Saviel Jr asanamwetsa chake chimodzi.

Isaac Mwase, wa timu ya Chihame, ntchito inamukulira pomwe anadzimwetsa yekha chigoli kuti zigoli za Civo zikwane zisanu.

Koma kuopa kudzangosilira nzinda wa Lilongwe, Chihame inamwetsa chigoli kudzera pa penate yomwe anamenya Pod Gondwe.

Zateremu ndekuti Civo yafika mu ndime ya ma timu 16 ndipo ikhale ikukumana ndi timu ya Abambo Robin Alufandika ya Mighty Tigers.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *