Colombia Yochepekedwayo Yapuntha Uruguay

Timu ya Colombia ndiyomwe ikumane ndi Argentina mundime yomaliza yachikho cha Copa America pamene timuyi yamenya Uruguay m’banda kucha walero mumasewero amundime yamatimu anai yampikisanowu.

Colombia yagonjetsa Uruguay ndichigoli chimodzi chomwe anamwetsa ndi Lerma pamphindi 39 zachigawo choyamba. Kumapeto kwachigawo choyambachi, osewera wa Colombia Munoz anapatsidwa chikalata chofiira atachita kusaweluzika.

Ngakhale kuti Colombia inasewera ochepa chigawo chonse chachiwiri, timuyi inakwanitsa kuteteza Chigolichi.Masewero atatha, kunabuka ndewu pakati pa otsatira Colombia komaso osewera ena a Uruguay monga Darwin Nunez wa Liverpool.

Mumasewero amundime yomaliza omwe alipo lamulungu ku USA, Colombia adzakumana ndi Argentina yomwe kuteteza chikhochi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *