Ifetu Takhumudwa Nanu A SULOM

Timu ya Moyale Barracks yati ndi yokhumudwa ndi ndikuchedwa kwa bungwe loyendetsa ligi ya TNM ya Super League of Malawi (SULOM) kuti ikakakamize timu ya Premier Bet Dedza Dynamos kuti ikonzetse bus yomwe otsatira timuyi anaphwanya ku Dedza pa 14 October chaka chatha.

Muchikalata chomwe Timveni Online yaona chomwe chasainidwa ndi mlembi wamkulu wa timuyi, Lieutenant Omega Masamba, chikuti osewera wawo Mcdonald Harawa, pa nthawiyo, yemwe pano anasiya mpira, anapatsidwa chilango atapezeka olakwa komanso timuyi inalipira K1.5million zomwe timuyi inachita.

Moyale yati ikufuna Sulom kuti iwonetse kusakondera powonetsetsa kuti timu ya Dedza yakonzetsa bus yawoyi komanso kupereka ndalama ya chipepeso kwa osewera omwe anavulala pa nthawiyo.

A Moyale ati ndi odabwa kuti bungweli lachita machawi pa nkhani yokhudza FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers pomwe maule anapereka ndalama pamwamba pokonzetsa bus ya Silver.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *