Kaliwo wanjatidwa kaamba kautambwali mu nzinda wa Blantyre

Rodrick Kaliwo wazaka 28 zakubadwa ali mmanja mwa apolisi pa mulandu obera athu powapusitsa kuti ndi sing’anga ochulukitsa ndalama komanso kuwasandutsa makhumutcha ku Bangwe munzinda wa Blantyre.

Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Limbe Aubrey Singanyama, mkuluyu yemwenso anamangidwapo m’mbuyomu, anapalamula mulanduwu pa 7 mwenzi omwewuno pomwe ananamiza mkulu wina ochita malonda m’dera lotchedwa Banana pomuwuza kuti apereke ndalama zokwana K60,000 yomwe amati ayichulukitsa kufika pa K900, 000 pakatha ma ola awiri (2 hours).

Iye wati a Kaliwo analephera kuchulukitsa ndalamayi ndipo m’malo mwake anawuzanso mwini ndalamayu kuti akatape dothi pa manda atsopano mdera lomweri, koma izi zinkayikitsa mwini ndalamayu ndipo anakatula nkhaniyi ku polisi komwe sanachedwe koma kukakwizinga unyolo sing’anga wachinyengoyu.

“Panthawi yomwe mkuluyu amamangidwa, anapezekanso ndi mulu wa zidutswa za mapepala ndi ufa wa phulusa okuda zomwe akuganiziridwa kuti amagwiritsa ntchito popusitsira anthu,” Singanyama watero.

Rodrick Kaliwo ndiwochokera m’mudzi mwa Mukoza kwa mfumu Makanjira m’boma la Mangochi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *