KB sikumvetsa pa Iponga

Mau oti pano mpakwathu anagona osadya aphelezera lero pomwe timu ya Kamuzu Barracks (KB), yafera pakwawo itapunthidwa ndi Iponga FC ya ku Karonga yomwe imasewera mu ligi ya Simso m’chigawo cha kumpoto.

Polingalira mtunda ochoka ku Karonga kufika ku Lilongwe, Walusungu Gondwe, anali ndi mayankho pa mphindi 90 za masewerowa pomwe anamwetsa chigoli cha Iponga FC.

Pomwe KB imadzifusa kuti pativuta mpati kuti mpaka tiyaluke chotere, oyimbira masewerowa anangoliza wenzulo kutsimikiza kuti zowonadi mamuna nzako mpachulu mkulinga utakwerapo.

Zateremu ndekuti Iponga FC yafika ndime yamatimu 16 ndipo ikhale ikukumana ndi Timu ya Mafco FC yomwe lero yapambana koma movutikira itachinya Soccer Rangers 1-0.

KB ili ndi ganyu ina lamulungu likudzali pomwe akhale akukumana ndi timu ya Silver Strikers yomwe nayo yatsanzikana ndi chikho cha FDH Bank Cup.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *