Ma Banker afika ku gym

Timu ya Silver Strikers yasainira m’gwirizano wopereka danga kwa osewera omwe achita bwino pa mwezi ‘player of the month’ kukapanga majowa-jowa komanso kulimbitsa thupi ndi kampani ya ‘Maybe Tomorrow Fitness’.

M’gwirizanowu ndi woti osewera omwe achita bwino pa mwezi adzikhala ma membala aku gym-yi ndipo adzikapanga chilichonse mwa ulele.

Mkulu wa Silver Strikers, Patrick Chimimba, wati mgwirizano umenewu uthandiza osewera kukhala athanzi zomwe zichepetse kuvulala pakati pawo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *