Malawi A Moto: Mitengo Ya Zinthu Ikukwera Molapisa

2 min read

Ena mwa aMalawi osauka omwe alire kwambiri ndi ganizo logwetsa ndalama ya kwacha

By Noel Mkwaila, BLANTYRE

Zavuta! Kwavuta! Moyo, maka wa aMalawi opeza mochepekedwa, ulimba kwambiri pomwe mitengo ya mafuta a galimoto, magetsi komanso paraffin yakwera modetsa nkhawa.

Izi zikutsatira ganizo la boma la Tonse logwetsa mphamvu ya kwacha ndi 44 kwacha pa 100 kwacha ili yonse. Ambiri alira mokweza!

Pomwe aMalawi adzuka lero, apeza bungwe la MERA lalengeza kuti petrol tsopano adzigulidwa pa K2530 pa lita kuchoka pa K1746.

Wapampando wa bungweli, Reckford Kampanje wati diesel tsopano wafika pa K2734 kuchoka pa K1920. Naye paraffin, yemwe okhala m’midzi ambiri amadalira, wafika pa K1910 kuchoka pa K1261.

Kuphatikiza apo, nawo magetsi afika pa K173.70 pa kilowati kuchoka pa K123.26. Awatu ndi magetsi omwe ESCOM inakwezanso mtengo ndi 18 percent mwezi wa August chaka chomwe chino.

Zatelemu ndiye kuti mitengo ya zinthu zina zambiri kuphatikizapo yokwelera galimoto monga minibus komanso zakudya ikwera.

Katswiri wa za ulamuliro wabwino, Mabvuto Bamusi akuti ichi ndi chipsinjo pa chipsinjo chimzake popeza zinthu zakhala zisakuyenda bwino kale. Iye wati aMalawi ayembekezere zokhoma.

Mmawu ake, mkulu wa bungwe la olemba anthu ntchito George Khaki akuti pali mantha kuti ena atha kuchotsedwa ntchito ndi momwe zililimu.

Zonsezi zikuchitika pomwe boma likusakasaka kupeza ndalama za thumba la Extended Credit Facility kuchokera ku bungwe la IMF lomwe likukumana posachedwapa.

Pakadalipano, President Lazarus Chakwera ali ku Saudi Arabia komanso apitilira ku Egypt ku mikumano yomwe akuti ithandiza kuchepetsa moto wa mavuto a chuma omwe ukuyaka mdziko lino.

.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours