---
title: "M’tengo wa pakete imodzi ya shuga, tsopano ukumafanana ndi wa bread m’modzi"
url: "https://malawifreedomnetwork.com/man-plans-to-ride-out-hurricane-florence-a-ride-hurricane/"
description: "ShareIzi zadza chifukwa bread wakwela mtengo kufika pa 1 000 Kwacha m’modzi , m’magolosale ena. Akuluakulu ena omwe ali ndi ma bakery, akuti mtengo wa tiligu, wakwela padziko lonse, zomwe zachititsanso kukwela kwa mtengo wa ufa opangila bread. “Chomcho , ufa wopangila bread wachoka pa 36, 000 Kwacha kufika pa 48, 000 Kwacha , thumba…"
author: "Suleman Chitera"
published: "2026-07-24T16:17:41+00:00"
modified: "2026-07-24T19:21:30+00:00"
language: "en-US"
type: "post"
site: "Malawi Freedom Network"
word_count: 89
---

# M’tengo wa pakete imodzi ya shuga, tsopano ukumafanana ndi wa bread m’modzi

Izi zadza chifukwa bread wakwela mtengo kufika pa 1 000 Kwacha m’modzi , m’magolosale ena.

Akuluakulu ena omwe ali ndi ma bakery, akuti mtengo wa tiligu, wakwela padziko lonse, zomwe zachititsanso kukwela kwa mtengo wa ufa opangila bread.

“Chomcho , ufa wopangila bread wachoka pa 36, 000 Kwacha kufika pa 48, 000 Kwacha , thumba limodzi la 50 kilograms,” watelo m’modzi mwa iwo.

Ndipo m’kulu wa bungwe la ogula malonda la Consumers Association of Malawi – CAMA, a John Kapito, wati boma lichitepo kanthu pa nkhani ya mitengoyi, chifukwa anthu m’dziko lino, avutika. “\`

---

Source: Malawi Freedom Network — https://malawifreedomnetwork.com/man-plans-to-ride-out-hurricane-florence-a-ride-hurricane/
