Maso athu ali kwa Maule enawa afera za eni

Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yathidzimula asilikali aku zomba a Cobbe Barracks pa masewero a ndime ya matimu 32 mu mpikisano wa chikho cha FDH Bank pa bwalo la Balaka.

Zigoli ziwiri zochokera kwa Gaddie Chirwa, komanso chimodzi cha Francisco Madinga, zinali zokwanira kusambitsa chokweza asilikaliwa.

Mu chigulu-gulu atatha masewerowa, sapota wina akuti ifetu tikufuna bullets awa afera za eni.

Zateremu ndekuti Manoma akhale akukumana ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ya matimu 16 mu chikhochi.

Pamasewero ena omwe analipo masanawa, Creck Sporting Club yapuntha FOMO FC kudzera kumapenate 3-1, pa mphindi 90 zitathera 2-2, pa bwalo la Civo.

Ndipo Premier Bet Dedza Dynamos yamenya Nyambadwe United ndi zigoli zitatu kwa ziwiri.

Pomwe timu ya Lube Masters, yomwe imasewera m’chigawo cha kumpoto mu Simso, yachapa anzawo a Sporting FC 1-0.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *