Maule alandira mphoto ya uchimo pa ziwawa

Bungwe la Super League of Malawi (Sulom) kudzera ku komiti yake yapadera yosungitsa mwambo lapereka chilango cha ndalama zokwana K2.3 million ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa ziwawa zomwe anachita oyitsatira timuyi pa 2 June 2024 pa bwalo la Kamuzu kutsatira kugonja ndi Timu ya Silver Strikers.

Chilangochi Chadza polingalira mfundo zingapo zomwe komitiyi inawunikira za momwe inayendera nkhaniyi.

Muchikalata chomwe bungweli latulutsa chikufotokoza kuti timu ya Bullets sinavute kuvomereza kulakwa kwawo pa zomwe zinachitika patsikuli.

Komiti yosungitsa mwamboyi yati inapereka milandu iwiri ku timu ya Bullets yomwe ndi kulephera kuletsa masapota kupanga zipolowe, komanso kubweretsa chisokonezo kumasewero a mpira wamiyendo.

Sulom yati pa chifukwa ichi komanso zomwe timuyi inachita popepesa timu ya Silver Strikers ndi kupereka K6 million yokonzera bus yomwe inaonongedwa pa tsiku la zipoloweli, kuthandizira kafuku-fuku wa nkhaniyi komanso kuphunzitsa achitetezo (stewards), ndizomwe zapangitsa kuwapatsa chilango chofewerako chonchi.

Komitiyi yati Sulom ikuyeneranso kumachita machawi akalandira uthenga okhudza nkhani ngati zimenezi komanso kufunika koti matimu adzikhala ndi udindo onena chiwerengero cha achitetezo omwe akufunika pa tsiku la masewero mogwirizana ndi malamulo a Police Act 115.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *