---
title: "Mbilizi ndi anzake atuluka pa belo"
url: "https://malawifreedomnetwork.com/mbilizi-ndi-anzake-atuluka-pa-belo/"
description: "Share Bwalo la magistrate ku Blantyre latulutsa pa belo yemwe anali wachiwiri kwa komishonala wa bungwe lotolela msonkho la MRA a Roza Mbilizi ndi anzawo ena awiri Anthuwa anawamanga kaamba kowaganizira kuti adagwiritsa ntchito molakwika nambala yopelekera msonkho (TPIN) ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Peter Mutharika. Bwaloli lalamula atatuwa kuti alipile K 350,000…"
author: "Suleman Chitera"
published: "2026-07-24T16:17:44+00:00"
modified: "2026-07-24T19:21:29+00:00"
language: "en-US"
type: "post"
site: "Malawi Freedom Network"
word_count: 79
---

# Mbilizi ndi anzake atuluka pa belo

Bwalo la magistrate ku Blantyre latulutsa pa belo yemwe anali wachiwiri kwa komishonala wa bungwe lotolela msonkho la MRA a Roza Mbilizi ndi anzawo ena awiri

Anthuwa anawamanga kaamba kowaganizira kuti adagwiritsa ntchito molakwika nambala yopelekera msonkho (TPIN) ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Peter Mutharika.

Bwaloli lalamula atatuwa kuti alipile K 350,000 ngati chikole komanso kuti apeleke ku bwaloli zikalata zawo zoyendera komanso anthuwa auzidwa kuti azikaonekera ku mafesi a ACB pa sabata ziwiri zili zonse

---

Source: Malawi Freedom Network — https://malawifreedomnetwork.com/mbilizi-ndi-anzake-atuluka-pa-belo/
