Messi Komaso Yamal Achita Bwino

Usiku walachiwiri komaso mmawa walero kunali masewero mumipikisano ya Euro 2024 komaso Copa America.

Usiku walachiwiri mumasewero amu Euro osewera wa Spain Lamine Yamal ndiyemwe anasankhidwa kuti anasewera bwino kuposa osewera onse pamene timu ya Spain yagonjetsa France ndizigoli ziwiri kwachimodzi kuti ifike mundime yomaliza yampikisanowu.

Ndipo m’banda kucha walero mumasewero amuchikho cha Copa America osewera wa Argentina Leonel Messi ndiyemwe anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa osewera onse pomwe Argentina yamenya Canada ndizigoli ziwiri kwachilowere kuti izigulire malo mundime yomaliza yampikisanowu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *