
Bishop Martin Mtumbuka wa dayosizi ya Karonga mumpingo waKatolika, walangiza Bishop Yohane Suzgo Nyirenda yemwe ndi othandizira Bishop wa Dayosizi ya Mzuzu kuti asamale ndi atsogoleri a ndale.
Bishop Mtumbuka wauza Bishop Nyirenda kuti ngati andale amuitana azipita, akamukonzera chakudya adye, akamukonzera chakumwa amwe koma asamanyamule zikwama zawo.
Mwambo odzoza Bambo Yohane Sugzo Nyirenda kukhala othandiza Bishop wa Mzuzu dayosizi uli mkati ku Mzuzu Stadium komwe kuli mtsogoleri wa dzikolino ndi wachiwiri wake.
Bishop dayosizi ya Mzuzu John Ryan ndiye adzonze Bambo Yohane Sugzo Nyirenda kukhala Bishop.