---
title: "Musapite Ku China: tizivutika tonse — Suleman"
url: "https://malawifreedomnetwork.com/musapite-ku-china-tizivutika-tonse-suleman/"
description: "Share Phungu wadera la Blantyre City South east Sammeer Suleman ati mtsogoleli wa dziko lino asapite ku China pa ulendo omwe wakonzedwa masiku akubwerawa. A Chakwera akuyembekezeka kupita m’dziko la China komanso Ku United States of America kuchoka pa 6 mpaka pa 9 September. Suleman ati mtsogoleli-yu akhale mdziko mommuno ndipo akhale ndi a Malawi…"
author: "Malawi Freedom Network"
published: "2026-07-24T16:17:51+00:00"
modified: "2026-07-24T19:21:21+00:00"
language: "en-US"
type: "post"
site: "Malawi Freedom Network"
word_count: 227
image: "https://malawifreedomnetwork.com/wp-content/uploads/2024/08/FB_IMG_1724856733860.jpg"
categories:
  - "Uncategorized"
---

# Musapite Ku China: tizivutika tonse — Suleman

Phungu wadera la Blantyre City South east Sammeer Suleman ati mtsogoleli wa dziko lino asapite ku China pa ulendo omwe wakonzedwa masiku akubwerawa.

A Chakwera akuyembekezeka kupita m’dziko la China komanso Ku United States of America kuchoka pa 6 mpaka pa 9 September.

Suleman ati mtsogoleli-yu akhale mdziko mommuno ndipo akhale ndi a Malawi pa nthawi yakukwera kwa mafutawa komanso zinthu zina.

Koma poyankhapo, mtsogoleli wa nyumbayi a Richard Chimwendo Banda ati nkofunika kuti mtsogoleli wa dziko lino apite ku China pofuna kuti ubale wa dziko lino ndi China upite patsogolo.

Iwo ati: “anthu akuvutika kale mdziko muno ndipo mkosafunika kuti mafuta a galimoto akwere.Boma lipeze njira zina zokonzera zinthu pa nkhaniyi.”

Suleman wapempha mkulu wabungwe la Consumers Association of Malawi(Cama) John Kapito kuti atule pansi udindo wake.

A Suleman omwe amayankhula kunyumba ya malamulo lachiwiri masana ati a Kapito alephera kutumikira a Malawi ngati mkulu wabungwe la Cama.

Izi zikudza pomwe a Kapito awuza nyumba zowulutsa mawu zina m’dziko muno kuti ndikoyenera kuti bungwe la Mera likweze mafuta a galimoto padakali pano pofuna kuti mafuta adzipezeka mosavuta.

Pomaliza kulankhula kwao a Sameer Suleman apempha mkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi, CAMA a John Kapito kuti atule pansi udindo wawo

A Suleman ati: “A Kapito akhalitsa pa udindowu.Kapito ndi mmodzi mwa anthu omwe anayambitsa nkhani yoti mafuta a galimoto akwere mdziko muno.”

---

Source: Malawi Freedom Network — https://malawifreedomnetwork.com/musapite-ku-china-tizivutika-tonse-suleman/
