Mzika zokhudzidwa zakhazikitsa kafukufuku pakugwa kwa ndege ya malemu Dr saulos chilima.

Ngati njira yoonetsetsa kuti apeze mayankha pamafunso okhudza kugwa kwa ndege yomwe inatenga moyo wa wachiwiri wamtsogoleri wadziko lino,Saulos chilima komanso anthu ena 8 Gulu lomwe likutchedwa kuti concerned citizens lati. Lakhazikitsa kafukufuku ofuna kudziwa chomwe chinadzetsa ngoziyi.

Muchikalata chomwe chasainidwa ndi a Edward kambaje, Oliver nakoma komanso a Osman Dagia ati gululi liri ndi mafunso osayankhika monganso mene ziliri kwa amalawi pamene boma likuyendetsera nkhaniyi.

Gululi lati likudabwa kuti mchifukwa chani mtsogoleri wadziko lino Lazarus chakwera anatenga maola 12 kuuza mtundu wa amalawi zakusowa kwa Ndege komanso mchifukwa chani anayamba kusaka ndege pro pomwe ndegeyo inasowa 10 koloko m’mawa.

“Kubisidwa pakafukufukuyu kukupereka mafunso kwa anthu ngati inali ngozi chabe kapena zochita kukonza”latero gululi.

Gululi lomwe lapempha dziko la America kuti alithandize ndi anthu odziwa kafukufuku lapemphenso amalawi kuti asataye mtima kamba koti posachedwapa zonse zidziwika.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *