Ntchito Ku Mabwalo A Milandu Zayima- Antchito Akunyanyala Ntchito

Olemba : Vincent Poya

Zinthu zayamba zayima kaye ku mabwalo a milandu pomwe anthu ogwira ntchito ayamba kunyanyala ntchito zawo.

Ena mwa ogwira ntchito a ku mabwalo a Blantyre high court komanso Lilongwe ananyamula zikwangwani pomwe alembapo nkhawa zawo.

Malingana ndi zomwe tapeza, momwe nthawi imati 6 koloko m’mawa lachinayi, pazipata komanso ma ofesi zinali zotseka ndi masamba.

Koma ku Blantyre sipanatenge nthawi pomwe apolisi anafika kumabwalowa komwe anachotsa masamba omwe anayikidwa ndi anthuwa poti malowa ali pafupi ndi malo omwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera amakatsegulira chionetsero cha zamalonda ku Trade fair grounds.

Yemwe akuyankhulira anthuwa a Charles Lizigeni auza olemba nkhani kuti kunyanyalaku kupitilira kufikira mbali yawo ndi ya boma zitagwirizana chimodzi.

Anthuwa mwazina akufuna boma liunikirenso malipiro awo apa mwezi komanso ndalama zawo zakutchuti zomwe ndi zochokera mchaka cha 2021 kufikira 2024.

Izi zikudza pambuyo pa zionetsero zomwe makontilakitala anachita masiku awiri apitawo pofuna kuumiriza bungwe loona za misewu ( Road Funds Administration) kuwapatsa ndalama zawo zokwana 14 biliyoni kwacha.

Pakadali pano a boma sanalankhulepo pa nkhaniyi ngakhale akuluakulu a ku mabwalo a milandu akukambilana ndi iyimilira ogwira ntchitowa pa tsogolo la nkhaniyi.

Related Posts

Malawi Freedom Network advice President Banda to fight corruption

If you thought Malawians are lazy people, I bet you a Dinosaur, think twice and you will know, check in Read more

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

Mustag Chothia, Sulema Ismael Karim In Land scam

Land remains one area that Malawians know has been heavily abused, characterised by ownership wrangles, not to mention corruption, fueled Read more

David Bisnowaty former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country

Political cum and former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country https://youtu.be/S20UYlVcHs8

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window