Ochita malonda ena akweza kwambiri mitengo yamafuta ophikira pamsika

Mwachitsanzo, ku Liwonde m’boma la Machinga mafuta a 1 lita tsopano akuwagulitsa pa K5, 500 kuchoka pa K3,500 ndipo malita awiri okwera kwambiri akuwagulitsa pa K10,495 kuchoka pa K7,500.

Ena mwa amalondawa ati akweza mitengo yamafuta ophikirawa kamba koti akusowa komanso momwe ndalama yadziko lino ikuyendera.

Bungwe lolimbikitsa chilungamo pamalonda la CFTC lachenjeza kuti lithana ndi amalondawa mogwiritsa ntchito lamulo latsopano loyendetsera malonda lomwe layamba kugwira ntchito pa 1 July chaka chino.

Mneneri wabungweli, a Innocent Helema wati sabata ino bungwe lawo lichita chipikisheni dziko lonse pofuna kupeza amalonda omwe akukweza mitengo yakatundu ofunikira kuphatikizapo mafuta ophikira.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *