Saviel Junior Wapsya Wa Ku Zambia

Katswiri osewera kutsogolo mu timu ya FCB Nyasa Big Bullets, yemwe amasewera pa ngongole ku timu ya Civil Service United (Civo), watsanzika ku timuyi ndipo akupita ku Zambia ku katumikira ku timu ya Mufulira Wanderers.

Saviel, wakhala ali ofunika kwambiri kutimu ya Civo pomwe wagoletsera zigoli 7 mu TNM Super League komanso posachedwapa wagoletsanso chigoli chotsanzikira ku timuyi pomwe Civo imasewera ndi Chihame All Stars mu mpikisano wa FDH Bank Cup.

Iye walemba pa tsamba lake la m’chezo la Facebook muchingelezi kuti ‘Thank you for the good time ma servants.’

Ndipo nayo Civo povomereza ya kutumulanso chingerezi chawo kuti ‘best of luck star.’

Saviel akhale akunyamuka m’dziko muno mawa lachinayi kupita ku banja la tsopano ku Zambia.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *