Silver yododa ija yatuluka mu FDH

Timu ya Silver Strikers yayenda wa uyo-uyo pa bwalo la Nankhaka mu nzinda wa Lilongwe, ataswedwa ndi timu ya Blue Eagles 5-3 pa mapenate, mu ndime ya matimu 32 a mpikisano wa FDH Bank Cup.

Pomwe mphindi 90 zimatha ndikuti matimu akufana mphamvu posagoletsana chigoli chili chonse.

Zinthu zinavuta kwambiri kumbali ya ma banker nthawi ya mapenote, pomwe otchinga pa golo la Blue Eagles, Joshua Waka, analumira mano pochotsa mpira wa Innocent Shema, kuti Blue Eagles ipambane 5-3.

Pamasewero ena timu ya FCB Nyasa Big Bullets ya philiphitha timu ya Bangwe All Stars ndi zigoli 5 kwa chilowere pa bwalo la Kamuzu mu nzinda wa Blantyre.

Pamene Moyale Barracks yasambitsa chokweza timu ya Chintheche United ndi zigoli 7 kwa 1 pamasewero omwe anali pa bwalo la Mzuzu.

Ndipo timu ya Karonga United yachapa Mzuzu City Hammers 2-1 pa bwalo la Karonga.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *