---
title: "STATE HOUSE ILENGEZA IMFA YA MIRIAM CHAKWERA"
url: "https://malawifreedomnetwork.com/state-house-ilengeza-imfa-ya-miriam-chakwera/"
description: "Share “`President Lazarus Chakwera wataya mlongo wawo Mirriam Chakwera yemwe wamwalira lero. Mlembi wa atolankhani a President Anthony Kasunda walengeza za imfa ya mlongo wake wa Chakwera mwachidule. A Kasunda adaonjeza kuti Chakwera wathetsa nthawi yomweyo zokambirana zake ndi anthu.“Mtsogoleri wa dziko lino ayambiranso zokambirana zake ndi anthu akayika maliro a mlongo wawo, zomwe zikuyenera…"
author: "Malawi Freedom Network"
published: "2026-07-24T16:17:41+00:00"
modified: "2026-07-24T19:21:30+00:00"
language: "en-US"
type: "post"
site: "Malawi Freedom Network"
word_count: 69
---

# STATE HOUSE ILENGEZA IMFA YA MIRIAM CHAKWERA

“\`President Lazarus Chakwera wataya mlongo wawo Mirriam Chakwera yemwe wamwalira lero.

Mlembi wa atolankhani a President Anthony Kasunda walengeza za imfa ya mlongo wake wa Chakwera mwachidule.

A Kasunda adaonjeza kuti Chakwera wathetsa nthawi yomweyo zokambirana zake ndi anthu. “Mtsogoleri wa dziko lino ayambiranso zokambirana zake ndi anthu akayika maliro a mlongo wawo, zomwe zikuyenera kuchitika pa Epulo 20 m’mudzi mwa Manase ku Mdika m’boma la Dowa,” adatero Kasunda.“\`

---

Source: Malawi Freedom Network — https://malawifreedomnetwork.com/state-house-ilengeza-imfa-ya-miriam-chakwera/
