
Mbiri Ya Moyo Wa Joseph Nkasa
Jimmy Joseph Kalekeni Nkasa anabadwa pa 3 DisembaIa mu 1967 m'boma la Zomba. Iye anabadwira m'dera lotchedwa Moleni ndipo ndi wachitatu kubadwa m'banja la ana anayi (amuna awiri ndi akazi awiri).
Katswiriyu anabadwira m'banja losauka zedi ndipo ali wachichepere amagwira maganyu n'cholinga choti azipeza zinthu zina m'moyo. Bambo ake anali woluka malichero ndi mabasiketi. Bambowa anaphunzitsa mwana waoyu lusoli ndipo anali kuthandizana kuti banja lizipeza chakudya.
M'zaka za m'ma 1970, makoIo ake anapeza maIo m'boma Ia Machinga. Banjali linakhazikika kwa mfumu yaikulu Sitola. Izi zinachititsa kuti boma la Machinga lisandukenso kwao.
Chifukwa chosowa chithandizo cha chuma, Joseph sanapite patali ndi sukulu. Iye anaisiya ali sitandade 8.
Nkasa anayamba kuyimba ali wachichepere mu ...