Friday, December 1Malawi's top news source
Shadow

Tag: Kasumbu Salima

ANTHU AYAMBA KUPALA WOKHA MISEWU

ANTHU AYAMBA KUPALA WOKHA MISEWU

Local
Atatopa ndikudikira kuti boma komanso andale awakonzere msewu olumikiza maboma a Dedza ndi Salima kudzera ku dera la Kasumbu, anthu okhala m'madera a Mfumu Madzumbi Nakaona, Chiwamba ,Ndembo ndi nzoola m'dela la Mfumu yayikulu Kasumbu ku Dedza akupala okha ndi makasu msewu wotalika makilomita 12 omwe ndioipa kwambiri. A Gulupu a Madzumbi atiuza kuti anaganiza zochita izi kaamba kakuti kwanthawi yaitali akhala akuvutika kwambiri popita ku msika kukagulitsa mbewu, komanso kukapeza zofunikira pa moyo wawo watsiku ndi tsiku. Iwo atinso chifukwa china nchakuti msewu akupalawu ndi wachidule kuyerekeza ndikuzungulira ku boma la Dedza koyenda ma ola 9. Mafumu ndi anthu kumeneko apempha akulu akulu kuti asiye kuwakumbukira nthawi ya chisankho yokha komanso kuthana mavuto omwe akukuman...