
YONECO iyendera anthu pa msasa wa anthu othawa madzi ku Mangochi
Olemba: Issa Prince Chimwala
Bungwe la Youthnet and Counseling (YONECO) lachiwiri linayendera anthu omwe akukhala pamsasa wa anthu othawa madzi osefukira kwa Chapola mdera la mfumu yaikulu Chimwala ku Mangochi. Pa Ulendowu, a Grant Dulla anapempha anthuwa pa msasawu kuti adzikondana komanso kukhulupirika kwa okondedwa awo.
"Nthawi ngati ino pamafunika kukondana pakati pa wina ndi nzake, mzanu ngati wachoka ndipo mwana wake anatsala ndipo akulira, msamaleni. Kwa anthu apabanja tikupempha kuti pakhale kukhulupirika. Sibwino kupita kunja mkumakapanga zibwezi chifukwa mapeto ake tidzatenganso matenda. Ife ngati bungwe la YONECO tidzibwera pamsasa pano kuonetsetsa kuti mukuthandizidwa moyenera". Anatsiriza choncho.
Pa ulendowu, a Dulla analinso ndi Issa Chimwala yemwe ndi ophunzitsa a...